Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 23:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Munthu wosauka ukamuweruza, usaweruze mokondera.

Onani mutuwo



Eksodo 23:3
10 Mawu Ofanana  

“Usakhotetse milandu ya anthu osauka.


Si kwabwino kukondera munthu woyipa pa milandu; kapena kupondereza munthu wosalakwa.


Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu,


Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo, kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,


“ ‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa osauka ndi olemera, koma muweruze mlandu wa mnzanu mwachilungamo.


Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.


Osamayangʼana nkhope poweruza koma muzimvetsera aangʼono ndi aakulu omwe chimodzimodzi. Musamaope munthu aliyense, pakuti chiweruzo ndi cha Mulungu. Muzindibweretsera mlandu uliwonse wovuta ndipo ndidzaumva.”


Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa.


Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.