Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 2:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anam'bisa miyezi itatu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, adamubisa miyezi itatu.

Onani mutuwo



Eksodo 2:2
8 Mawu Ofanana  

Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.


Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo.


Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.


Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo.


“Pa nthawi imeneyo Mose anabadwa, ndipo anali wokongola kwambiri. Iye analeredwa mʼnyumba ya abambo ake kwa miyezi itatu.


ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto. Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe, wapaderadera pakati pa abale ake.


Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.


Choncho anatuma munthu kukamutenga ndipo anabwera naye. Iye anali wofiirira, wa maonekedwe abwino ochititsa kaso. Ndipo Yehova anati, “Mudzoze popeza ndi ameneyu.”