Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze.
Eksodo 10:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati ukana kuwalola, ndigwetsa dzombe mʼdziko lako lino mawa. Buku Lopatulika pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukakanabe kuŵalola kuti apite, ndikugwetsera dzombe maŵa m'dziko mwako. |
Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze.
Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu.
Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ”
Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ”
Farao anati, “Mawa.” Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu.
Ndidzasiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chizindikiro chozizwitsa ichi chidzachitika mawa.”
Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero.
“Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe, dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono, dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka; gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga.
Ndipo mʼkati mwa utsimo munatuluka dzombe kukalowa mʼdziko lapansi ndipo linapatsidwa mphamvu zoluma ngati za zinkhanira pa dziko lapansi.