Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110
Eksodo 1:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu onse obadwa mwa Yakobo analipo 70. Yosefe nʼkuti ali kale ku Igupto. Buku Lopatulika Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali mu Ejipito. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali m'Ejipito. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chiŵerengero chenicheni cha anthu obadwa mwa Yakobe chinali makumi asanu ndi aŵiri. Yosefe anali atakhazikika kale ku Ejipito. |
Yosefe anakhala mu Igupto pamodzi ndi banja lonse la abambo ake. Anakhala ndi moyo zaka 110
Kotero Mulungu anawakomera mtima azambawo, ndipo Aisraeli anapitirirabe kuchulukana nakhala amphamvu kwambiri.
Izi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75.
Makolo anu amene anapita ku Igupto analipo makumi asanu ndi awiri onse pamodzi, ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.