Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
Eksodo 1:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tiyeni tiwachenjerere. Tikapanda kutero adzachuluka kuposa ife, ndipo ngati kutakhala nkhondo, adzadziphatika kwa adani athu nadzamenyana nafe, kenaka nʼkudzachoka mʼdziko muno.” Buku Lopatulika Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mvetsani tsono, ife tichite nawo mwanzeru anthu ameneŵa. Tiŵachenjerere, kuti asachuluke, chifukwatu pa nthaŵi ya nkhondo, iwoŵa angathe kudzaphatikizana ndi adani athu, nadzalimbana nafe, kenaka nkudzachoka m'dziko mwathu muno.” |
Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.
Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka, amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.
amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake, kukonzera chiwembu atumiki ake.
Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”
Kutacha Ayuda ena anakonza chiwembu ndipo analumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo.
Mfumuyo inachita mwachinyengo ndi mtundu wathu ndi kuwazunza kuti ataye ana awo akhanda kuti afe.
Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa?