Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 1:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Awa ndi mayina a ana a Israeli amene anapita ku Igupto pamodzi ndi Yakobo abambo awo, aliyense ndi banja lake:

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Naŵa ana a Yakobe amene adapita ku Ejipito pamodzi ndi Yakobeyo ndi mabanja ao omwe:

Onani mutuwo



Eksodo 1:1
15 Mawu Ofanana  

Pamene Mulungu anaona kuti Yakobo sankamukonda Leya kwambiri, Iye analola kuti Leya uja akhale ndi ana, ndi kuti Rakele akhale wosabala.


Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.


Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.


Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda;


Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo.


“Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.