Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 8:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pamene ndinali kulingalira za zinthu zimenezi, mwadzidzidzi mbuzi yayimuna inatulukira cha kumadzulo, kudutsa dziko lonse lapansi mwaliwiro ikuyenda mʼmalele mokhamokha. Mbuzi yayimunayo inali ndi nyanga yayikulu pakati pa maso ake.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pamaso ake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ake.

Onani mutuwo



Danieli 8:5
7 Mawu Ofanana  

Kenaka mfumu yamphamvu idzafika imene idzalamulira ndi ufumu waukulu ndi kuchita zimene ifuna.


Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa.


“Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi.


“Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire.


Mbuzi yayimuna ija ndi mfumu ya Agriki, ndipo nyanga yayikulu pakati pa maso ake aja ndi mfumu yoyamba.


Inabwera molunjika nkhosa yayimuna ya nyanga ziwiri ija imene ndinaona itayima pafupi ndi mtsinje. Ndipo inayithamangira mwaukali.


Mbuziyo inayamba kudzikuza kwambiri chifukwa cha mphamvu zake koma pamene mphamvuzo zinakula kwambiri nyanga yake yayikulu inathyoka, ndipo mʼmalo mwake panamera nyanga zinayi moloza mbali zonse zinayi.