Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’ ”
Danieli 8:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinaona nkhosa yayimunayo ikuthamanga mwaukali kupita kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. Palibe chirombo chimene chikanatha kulimbana nayo, ndipo palibe akanatha kulanditsa kanthu kwa iyo. Iyo inachita monga inafunira ndipo inali ndi mphamvu zambiri. Buku Lopatulika Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa. |
Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’ ”
ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?
Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu; kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali,
Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija.
“Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika.
Chifukwa cha udindo waukulu umene anapatsidwanso, anthu onse ndi mitundu ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana ankanjenjemera ndikumuopa iye. Amene mfumu inafuna anawaphadi; amene inafuna kuwasunga, inawasunga; amene inafuna kuwakweza, inawakweza; ndipo amene inafuna kuwatsitsa, inawatsitsa.
“Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’
Inafika pafupi ndipo inalimbana nayo mwaukali nkhosa yayimuna ija nʼkuthyola nyanga zake ziwiri. Nkhosa yayimunayo inalibenso mphamvu zogonjetsera mbuziyo; choncho mbuzi ija inagwetsa nkhosayo pansi nʼkuyipondaponda, ndipo palibe akanatha kulanditsa nkhosayo kwa mbuziyo.
Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu, mʼgulu la anthu a mitundu yambiri, ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango. Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa, amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula, ndipo palibe angathe kuzilanditsa.
Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa; nyanga zake zili ngati za njati. Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina, ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi. Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu; nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”