Danieli 5:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho mfumu Belisazara anachita mantha koposa ndipo nkhope yake inapitirira kusinthika. Akalonga ake anathedwa nzeru. Buku Lopatulika Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru. |
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera, ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti: Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo, ndipo manja anthu alefukiratu. Nkhawa yatigwira, ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
Choncho ndinatsala ndekha, ndikuonetsetsa masomphenya a ulemererowa. Ndiye nkhope yanga inasinthika, ndinalefuka, ndipo ndinalibenso mphamvu.
Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona.
Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu.
Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri.