Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake.
Danieli 5:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lina mfumu Belisazara anakonza phwando lalikulu la akalonga ake 1,000 ndipo anamwa vinyo pamodzi ndi iwo. Buku Lopatulika Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake aakulu chikwi chimodzi madyerero aakulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake akulu chikwi chimodzi madyerero akulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho. |
Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake.
ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye.
Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi; kumeta mutu wanu mpala ndi kuvala ziguduli.
Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
Yehova akuti, “Imfa yalunjika pa Ababuloni, pa akuluakulu ake ndi pa anthu ake a nzeru!
Ngati achita dyera ndiye ndidzawakonzera madyerero ndi kuwaledzeretsa, kotero kuti adzasangalala, kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,” akutero Yehova.
Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake, abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo; adzagona kwamuyaya osadzukanso,” akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo; adzatenthedwa ngati ziputu zowuma.