Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”
Danieli 3:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! Buku Lopatulika Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. |
Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”
Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”
Mfumukazi, pakumva mawu a mfumu ndi akalonga ake, analowa mʼchipinda cha phwando ndipo anati, “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Musavutike! Nkhope yanu isasinthike!
Choncho akalonga ndi nduna pamodzi anapita kwa mfumu ndipo anati: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo wautali!
Mubwezereni aliyense amene munamukongola. Ngati inu muli ndi ngongole yamsonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira. Ngati ndi kuopa perekeni kwa oyenera kuwaopa ndipo ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu.