Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 3:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati:

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara.

Onani mutuwo



Danieli 3:3
11 Mawu Ofanana  

Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija.


ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto.


“Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse


Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira, palibe amene amafunafuna Mulungu.


Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho.


Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.