Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 2:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.”

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake.

Onani mutuwo



Danieli 2:6
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru.


Mwa lamulo la Belisazara, Danieli anavekedwa chovala cha pepo, mkanda wagolide unayikidwa mʼkhosi mwake, ndipo analengeza kuti anali wachitatu mu ulamuliro mu ufumuwo.


Mfumu inafuwula kuyitana owombeza, alawuli ndi amawula kuti abwere. Ndipo anawawuza anthu anzeru a ku Babuloni kuti, “Aliyense amene awerenge malembawa ndi kundiwuza tanthauzo lake adzavekedwa chovala cha pepo ndi mkanda wa golide udzavekedwa mʼkhosi mwake, ndipo adzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”


chifukwa ndidzakulipira bwino kwambiri ndipo ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene. Bwera ndipo uwatemberere anthu amenewa mʼmalo mwanga.’ ”


Balaki anati kwa Balaamu, “Kodi sindinakutumizire uthenga woti ubwere msanga? Chifukwa chiyani sunabwere kwa ine? Kodi sindingathe kukulipira mokwanira?”


Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.


Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”