Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.
Danieli 2:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi. Buku Lopatulika Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu padziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse. |
Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.
Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu,
Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa,
Pamene amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula anabwera, ndinawafotokozera maloto, koma sanathe kunditanthauzira.