Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 2:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.

Onani mutuwo



Danieli 2:1
14 Mawu Ofanana  

Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere.


Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni.


mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.”


Chandikomera kukuwuzani zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wammwambamwamba wandichitira.


Ndili chigonere pa bedi langa, ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Zinthu ndi masomphenya zimene ndinaziona zinandiopsa.


Choncho mfumu Belisazara anachita mantha koposa ndipo nkhope yake inapitirira kusinthika. Akalonga ake anathedwa nzeru.


Kenaka mfumu inabwerera ku nyumba yake ndipo inakhala usiku wonse osadya kanthu, osalola chosangalatsa chilichonse. Ndipo sinagone tulo.


Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.


“Ine Danieli ndinavutika mu mzimu, ndipo zimene ndinaziona mʼmasomphenya zinandisautsa mʼmaganizo.