Nditamva zimenezi, ndinakhala pansi ndi kuyamba kulira. Ndinalira kwa masiku angapo. Ndinkasala zakudya ndi kumapemphera pamaso pa Mulungu Wakumwamba.
Danieli 10:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu. Buku Lopatulika Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu. |
Nditamva zimenezi, ndinakhala pansi ndi kuyamba kulira. Ndinalira kwa masiku angapo. Ndinkasala zakudya ndi kumapemphera pamaso pa Mulungu Wakumwamba.
Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa, “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?”
Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani?
“Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye, inu nonse amene mumakonda Yerusalemu, kondwera nayeni kwambiri, nonse amene mumamulira.
Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi, ndi maso anga ngati kasupe wa misozi! Ndikanalira usana ndi usiku kulirira anthu anga amene aphedwa.
Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo.
Yesu anayankha kuti, “Kodi oyitanidwa ku ukwati angamalire bwanji pamene mkwati ali naye pamodzi? Nthawi idzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa ndi pamene adzasala kudya.”
Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni.
Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo.