Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira.
Afilipi 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu. Buku Lopatulika Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. |
Koma ayamikidwe Mulungu pakuti ngakhale munali akapolo a tchimo, munamvera ndi mtima wonse chiphunzitso chimene munalandira.
Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu.
Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu?
Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe.
Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.