mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse, ameneyo adalitse anyamata awa. Kudzera mwa iwowa dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka. Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu pa dziko lapansi.”
2 Samueli 4:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayankha Rekabu ndi mʼbale wake Baana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene wandipulumutsa ku mavuto anga onse, Buku Lopatulika Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Davide adayankha Rekabu ndi Baana mbale wake kuti, “Ndithu pali Chauta wamoyo, amene waombola moyo wanga kwa adani anga onse, |
mngelo amene wandipulumutsa ine ku zovuta zonse, ameneyo adalitse anyamata awa. Kudzera mwa iwowa dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abrahamu ndi Isake, adzamveka. Iwowa adzakhala ndi ana ambiri nadzasanduka mtundu waukulu pa dziko lapansi.”
Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini,
Tsono mfumu inalumbira kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene anandipulumutsa ine ku mavuto onse,
amene awombola moyo wako ku dzenje ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe pamene ndidzayimba matamando kwa Inu amene mwandiwombola.
Monga momwe ine lero ndachitira kuwuyesa moyo wanu ngati wamtengowapatali, momwemonso Yehova awuyese moyo wanga wamtengowapatali ndipo andipulumutse mʼmavuto anga onse.”