Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 2:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli.

Onani mutuwo

Buku Lopatulika

Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero Davide adapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake aŵiri aja, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimele.

Onani mutuwo



2 Samueli 2:2
5 Mawu Ofanana  

Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;


Davide anakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi ankhondo ake, aliyense ndi banja lake. Davide ali ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wamasiye wa Nabala.


Akazi awiri a Davide, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli anatengedwanso.