Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.
2 Samueli 1:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.” Buku Lopatulika Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adamufunsa kuti, “Ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndathaŵa ku zithando zankhondo za Aisraele.” |
Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo.
Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?” Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.”
Kenaka analowa mʼnyumbamo nakayima pamaso pa mbuye wake Elisa. Elisa anafunsa kuti, “Kodi Gehazi unali kuti?” Iye anayankha kuti, “Mtumiki wanu sanapite kwina kulikonse.”
Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo.