Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.
Zekariya 9:1 - Buku Lopatulika Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Katundu wa mau a Yehova pa dziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mau a Chauta akudzudzula dziko la Hadaraki, ndiponso mzinda wa Damasiko. Paja mizinda yonse ya ku Aramu njake ya Chauta, chimodzimodzi ngati mafuko onse a Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki ndi mzinda wa Damasiko pakuti maso a anthu ndiponso mafuko onse a Israeli ali pa Yehova— |
Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.
Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.
Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.
wamkulu mu upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;
Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi mu Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.
Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse.
Ndidzalitulutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yake, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yake ndi miyala yake.