koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.
Zekariya 8:7 - Buku Lopatulika Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, Ndidzapulumutsa anthu anga amene ali ku maiko akuvuma ndi akuzambwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani ndidzapulumutsa anthu anga kuchokera ku mayiko a kummawa ndi kumadzulo. |
koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Taonani, awa adzachokera kutali; ndipo taonani, awa ochokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ochokera kudziko la Asuwani.
Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.
Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno.
Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.
Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukuchotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'mizindamo; ndi pamabwinja padzamangidwa.
Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.
Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.