Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Zekariya 8:5 - Buku Lopatulika

Ndi m'miseu ya mzinda mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akusewera m'miseu yake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndi m'miseu ya mudzi mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akusewera m'miseu yake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo m'miseu ya mumzindamo mudzadzaza ndi ana, anyamata ndi atsikana, amene azidzaseŵeramo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo misewu ya mu mzindamo idzadzaza ndi anyamata ndi atsikana akusewera.”

Onani mutuwo



Zekariya 8:5
11 Mawu Ofanana  

Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.


Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.


mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.


Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.


nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.