Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.
Zekariya 8:2 - Buku Lopatulika Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Mtima wanga wonse uli pa Ziyoni, anthu ake ndimaŵakonda mwansanje kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndikuchitira nsanje yayikulu Ziyoni. Mtima wanga ukupweteka chifukwa cha nsanje pa iyeyo.” |
Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.
Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda.
Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.
Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera chilango; Yehova ndiye wobwezera chilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera chilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ake.
Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.