Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,
Zekariya 7:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunachitika chaka chachinai cha mfumu Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lachinai la mwezi wachisanu ndi chinai, ndiwo Kisilevi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunachitika chaka chachinai cha mfumu Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lachinai la mwezi wachisanu ndi chinai, ndiwo Kisilevi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa chaka chachinai cha ufumu wa Dariusi, tsiku lachinai la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa Zekariya uthenga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa chaka chachinayi cha Mfumu Dariyo, pa tsiku lachinayi la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi Zekariya. |
Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,
Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wachisanu ndi chinai, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti,
Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yachiwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti,
Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,