Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Zekariya 6:7 - Buku Lopatulika

Ndi amphamvuwo anatuluka nayesa kunka kuyendayenda m'dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m'dziko. Momwemo anayendayenda m'dziko.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndi amphamvuwo anatuluka nayesa kunka kuyendayenda m'dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m'dziko. Momwemo anayendayenda m'dziko.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akavalowo atatuluka, anali ndi phamphu kufuna kuyendera dziko lonse lapansi. Iye uja adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dziko lapansi.” Akavalowo adapitadi kukayendera dziko lapansi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pamene akavalo amphamvuwa ankapita, anali ndi changu chofuna kuyendera dziko lapansi. Ndipo iye anati, “Pitani, kayendereni dziko lapansi!”

Onani mutuwo



Zekariya 6:7
8 Mawu Ofanana  

Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.


Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake;


Kunena za nyanga khumi, mu ufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pao idzauka ina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzachepetsa mafumu atatu.


Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko.


Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo.