Zekariya 5:9 - Buku Lopatulika Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati padziko ndi thambo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nditayang'ananso, ndidaona akazi aŵiri okhala ndi mapiko onga a kakoŵa. Akaziwo ankabwera chouluka ndi mphepo. Adanyamula gondolo lija, kupita nalo pakati pa dziko lapansi ndi mlengalenga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona akazi awiri akuwuluka kubwera kumene kunali ine; akuwuluzika ndi mphepo. Iwo anali ndi mapiko ngati a kakowa, ndipo ananyamula dengu lija, kupita nalo pakati pa mlengalenga ndi dziko lapansi. |
Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake; ndipo njiwa ndi namzeze ndi chingalu ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa chiweruziro cha Yehova.
Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa.
Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;
Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;