Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Zekariya 5:6 - Buku Lopatulika Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidafunsa kuti, “Kodi nchiyani?” Iye adati, “Chimenechi ndi gondolo loyesera, ndipo likutanthauza uchimo wa anthu m'dziko lonse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndinafunsa kuti, “Kodi chimenechi nʼchiyani?” Mngeloyo anayankha kuti, “Limeneli ndi dengu loyezera.” Ndipo anawonjezera kunena kuti, “Umenewu ndi uchimo wa anthu mʼdziko lonse.” |
Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;
kuti tigule osauka ndi ndalama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu.
Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao?
Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.
ndipo taonani, chozunguniza chantovu chotukulidwa: ndipo ichi ndi mkazi wokhala pakati pa efa.