Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.
Zekariya 4:8 - Buku Lopatulika Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adandipatsanso uthenga uwu wakuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anayankhulanso nane kuti, |
Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao.
Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu.
Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu.