Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Zekariya 4:5 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mngeloyo adayankha kuti, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidati, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?” Ndinayankha kuti, “Ayi mbuye wanga.” |
Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.
Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.
Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani.
Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo take.
Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziyani mbuyanga?