Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Zekariya 4:3 - Buku Lopatulika

ndi mitengo iwiri ya azitona pomwepo, wina kudzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina kudzanja lake lamanzere.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi mitengo iwiri ya azitona pomwepo, wina kudzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina kudzanja lake lamanzere.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambali pake pa choikaponyalecho pali mitengo iŵiri ya olivi, wina ku dzanja lamanja, wina ku dzanja lamanzere.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndiponso pambali pake pali mitengo ya olivi iwiri, umodzi uli kumanja kwa mbaleyo ndipo winawo kumanzere.”

Onani mutuwo



Zekariya 4:3
7 Mawu Ofanana  

chingwe chasiliva chisanaduke, ngakhale mbale yagolide isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanathyoke kuchitsime;


Pamenepo anati, Awa ndi ana aamuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi.


Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,


Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wakuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?


Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.


Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?