Zekariya 4:2 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;
Onani mutuwo
Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikapo nyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;
Onani mutuwo
Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira.
Onani mutuwo
Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira.
Onani mutuwo