Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?
Zekariya 4:13 - Buku Lopatulika Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iye adati, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidayankha kuti, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?” Ine ndinati, “Ayi mbuye wanga.” |
Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?
Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziyani mbuyanga?
Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga.