Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?
Zekariya 4:11 - Buku Lopatulika Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa choikaponyali nchiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa choikapo nyali nchiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidamufunsa munthuyo kuti, “Nanga mitengo iŵiri ya olivi ili kumanja ndi kumanzere kwa choikaponyalecho ikutanthauza chiyani?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka ndinafunsa mngelo uja kuti, “Kodi mitengo ya olivi iwiri ili kumanja ndi kumanzere kwa choyikapo nyalechi ikutanthauza chiyani?” |
Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide?
ndi mitengo iwiri ya azitona pomwepo, wina kudzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina kudzanja lake lamanzere.
Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.