Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.
Zekariya 4:10 - Buku Lopatulika Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa. “Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli. (“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”) |
Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.
Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching'ono, chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mawere a zitonthozo zake; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wake.
Ndipo mudzachiona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ake, ndipo adzakwiyira adani ake.
Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.
Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Ndipo kunachitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala chilili bwanji? Popeza ndiye wamng'ono.
Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, lekanitu; Yakobo adzakhala chilili bwanji? Pakuti ali wamng'ono.
Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi mu ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe?
Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pamwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.
Katundu wa mau a Yehova padziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele;
Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.
Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse.
Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.