Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.
Zekariya 3:5 - Buku Lopatulika Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mngelo uja adauza omperekeza aja kuti, “Mvekeni nduŵira yabwino.” Motero adamuveka nduŵira yabwino pa mutu, namuvekanso zovala zatsopano. Nthaŵiyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pomwepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali. |
Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira.
Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.
Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.
ndipo utenge siliva ndi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe;
akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena,
Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide.