Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Zekariya 2:7 - Buku Lopatulika

Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babiloni.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babiloni.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tiyeni, thaŵirani ku Ziyoni, inu amene mudatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Tuluka, iwe Ziyoni! Thawa, iwe amene umakhala mʼdziko la mwana wamkazi wa Babuloni!”

Onani mutuwo



Zekariya 2:7
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.


Tulukani inu mu Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo.


Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.


Dzisanse fumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.


Thawani pakati pa Babiloni, tulukani m'dziko la Ababiloni, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.


Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova.


Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.


Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.


Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.


Ndipo Aisraele onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kufuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.


Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;