Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
Zekariya 2:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyo adzamtenganso Yuda kuti akhale chuma chake m'dziko lopatulika, ndipo Yerusalemu adzakhala mzinda wake wapamtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova adzachititsa kuti Yuda akhale chuma chake mʼdziko lopatulika ndipo adzasankhanso Yerusalemu. |
Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.
Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.
Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.
Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanache, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.
iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kuchokera m'ngodya zake, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaye kunja;
Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusiridwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.
Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Mizinda yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.
Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?
Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso.