Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Zekariya 2:1 - Buku Lopatulika

Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m'dzanja lake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m'dzanja lake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndidaonanso zinthu m'masomphenya: ndidaona munthu atatenga chingwe choyesera m'manja mwake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona munthu atanyamula chingwe choyezera mʼmanja mwake.

Onani mutuwo



Zekariya 2:1
12 Mawu Ofanana  

Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.


Ndipo chingwe choyesera chidzatulukanso kulunjika ku chitunda cha Garebu, ndipo chidzazungulira kunka ku Gowa.


Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova.


Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m'dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye.


Ndipo taonani, panali linga kunja kwake kwa nyumba ya Kachisi poizinga, ndi m'dzanja lake la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uliwonse mkono kudza chikhato; ndipo anayesa chimangidwecho kuchindikira kwake bango limodzi, ndi msinkhu wake bango limodzi.


Potuluka munthuyu kunka kum'mawa ndi chingwe choyesera m'dzanja lake, anayesa mikono chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo.


Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'chuuno.


Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.


Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.


Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai.


Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.


Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nao muyeso, bango lagolide, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake.