Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu;
Zekariya 13:5 - Buku Lopatulika koma adzati, Sindili mneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma adzati, Sindili mneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma adzati, ‘Sindine mneneri ai. Ndine mlimi, poti ndakhala ndikulima munda kuyambira ubwana wanga.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’ |
Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu;
Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza chiyani? Adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.