Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango yakuthengo la kumwera kwa Yuda;
Zekariya 11:2 - Buku Lopatulika Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lirani mokweza, inu mitengo ya paini, pakuti mikungudza yagwa, mitengo yamphamvu yaonongeka. Lirani mokweza inu mitengo ya thundu ya ku Basani, pakuti nkhalango yoŵirira ija aiyeretsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa; mtengo wamphamvu wawonongeka! Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani; nkhalango yowirira yadulidwa! |
Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango yakuthengo la kumwera kwa Yuda;
Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu.
Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu.
Tsoka osalabadirawo mu Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!
Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa.