Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali, kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza.
Zekariya 10:3 - Buku Lopatulika Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuti, “Ndaŵakwiyira kwambiri abusa, ndipo atsogoleri a m'dzikomo ndidzaŵalanga. Koma Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidzasamala nkhosa zanga, ndiye kuti banja la Yuda, ndipo ndidzazisandutsa ngati akavalo ankhondo amphamvu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndawakwiyira kwambiri abusa, ndipo ndidzalanga atsogoleri; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira nkhosa zake, nyumba ya Yuda, ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo. |
Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali, kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza.
Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.
Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.
Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu lakumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi.
Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika.
chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala;
Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.
Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika.
Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma.
Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna.
Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.
Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?
Ndipo akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu.
Ndipo kudzachitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akuvala chovala chachilendo.
Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.
Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.
Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.
Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya.