Zekariya 1:9 - Buku Lopatulika Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndiye ine ndinamufunsa kuti, ‘Mbuye wanga, kodi nchiyaninso chikatere?’ Mngelo amene ankalankhula nane anayankha kuti, ‘Ndikufotokozera tanthauzo lake.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?” Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, “Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani.” |
Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi:
Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.
Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anatuluka, ndi mthenga wina anatuluka kukomana naye,
Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo take.
Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa choikaponyali nchiyani?
Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anatuluka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nchiyani ichi chilikutulukachi.