Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!
Zekariya 1:5 - Buku Lopatulika Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? |
Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yehowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!
Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amowabu analowa m'dziko poyambira chaka.
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja;
fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.
Tenganso mpukutu wina, nulembe m'menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha.
Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.
Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;
Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.