kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.
Zekariya 1:12 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi mizinda ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mngelo wa Chautayo anafunsa kuti, ‘Inu Chauta Wamphamvuzonse, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya ku Yuda imene mudaikwiyira pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, mudzakhalabe oiwumira mtima mpaka liti?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?” |
kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri.
Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?
Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.
Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.
Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.
Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mzinda udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe.
Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pamadzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?
chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.
Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva Inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa.
Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.
Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi?
kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.
ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?