Zefaniya 2:6 - Buku Lopatulika Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala busa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala busa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dziko limene lili m'mphepete mwa nyanja, lidzasanduka madambo a abusa, ndi makola a nkhosa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti, lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa. |
Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo.
Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako chifukwa cha kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng'ombe ndi popondaponda nkhosa.
Yehova wa makamu atero: M'malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m'mizinda yake yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao.
Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.