Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.
Zefaniya 2:13 - Buku Lopatulika Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adzasamulira dzanja lake kumpoto ndi kuwononga dziko la Asiriya. Mzinda wa Ninive adzausandutsa bwinja, udzakhala wagwaa ngati chipululu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova adzatambasulira dzanja lake kumpoto ndi kuwononga Asiriya, kusiya Ninive atawonongekeratu ndi owuma ngati chipululu. |
Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.
Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.
Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.
Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.
Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.
Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.
Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe.
Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza?
Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala mu Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;