pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.
Yoweli 3:21 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala m'Ziyoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzalipsira magazi a ophedwawo, sindidzalekerera tchimo la olakwawo. Ine Chauta ndimakhala ku Ziyoni.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululuke ndidzakhululuka.” Yehova amakhala mu Ziyoni! |
pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.
Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.
Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mzindawo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.
Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.
Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,
Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;