Tayang'ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.
Yoweli 3:20 - Buku Lopatulika Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ku Yudako kudzakhala anthu mpaka muyaya, ndipo ku Yerusalemu sikudzatha anthu pa mibadwo yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yuda adzakhala ndi anthu mpaka muyaya ndi Yerusalemu ku mibadomibado. |
Tayang'ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.
Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.
Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.