Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Yoweli 3:16 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu; dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka. Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake, linga la anthu a ku Israeli. |
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.
Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.
Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.
Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele;
Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo.
Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.
Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.
Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;
ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.
Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.
Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.
amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.
Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.
Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.
ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.
Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.